spot_img
Wednesday, January 22, 2025
More
    HomeLatestZINAYENDA BWANJI KU MZUZU? KUSANTHULA UTM CONVENTION

    ZINAYENDA BWANJI KU MZUZU? KUSANTHULA UTM CONVENTION

    -

    Msonkhano waposachedwapa wa UTM, umene unachitikira ku Mzuzu ndipo ndikusankha Dr. Dalitso Kabambe kukhala mtsogoleri wa chipanichi, wasiya anthu ambiri atamangidwa mphukusi. Msokhanowu, maka zotsatila za zisankhozi zadzetsa mafunso ambiri omwe mpaka pano mayankho zakupezeka.

    Enafe sitinali muchpinda momwe msonkhanowu umachitikira poti sitinali ma deligeti, koma tili panja tinamvako kuti magetsi anali vuto maka mmene anthu anali kuwerengera mavoti. Onenawo akuti magetsiwa anazima kokwana kasanu ndi kamodzi. Mpaka pano palibe wina aliyense wa ku chipani kapena kwa awo amayendetsa zisankhozi amene wafotokozapo kuti chimachitika ndi chani.

    Nkhani ina imene ikuoneka kuti anthu akungoyilambalala ndikusiyana kwa namabla ya anthu omwe anavota pa mtsogoleri wa chipanichi ndi awo amene anavota mipando yosiyanasiyana.

    Mukaundula munaonetsa kuti anthu 748 ndi amene amayenera kuvota patsikuli ndipo pa mipando yonse inaonetsa kuti anthu awawa anavotadi koma chodabwitsa ndi chakuti pa mpando wa mtsogoleri ma voti onse owerengedwa kuchotsa owonongeka anakwana 727 pamene owonongeka anali 9. Ngakhale zonsezi zinali choncho anthuwa amavota kugwiritsa njira ya ka bunkhu komwe kanali ndi masamba 11 kuyimira maudindo onse kumphatikiza a mtsogoleri wa chipani. Mpaka lero palibe wa kuchipani kapena mmodzi mwa awo amene amayendetsa zisankho wafotozapo kuti kodi mavoti 12 anapita kuti.

    Kwa aliyense okonda UTM komaso okonda Malawi izizi zikudzetsa mafunso kuti kodi chpani cha UTM chomwe chimayimira polimbikitsa chilungamo, kusintha pakachitidwe kandale komanso kuchita zinthu mokomera ali yense, chikuchitadi monga chinenera. Chodetsa nkhawa kwambiri ndi chakuti amtsogoleri atsopano achipanichi angoyang’ana kumbali pakhani zimenezi and kwaiwo sakuonapo vuto.

    Nkhani ina yomwe yaponyedwa kuchipinda ndiyakuti oyendetsa chisankhochi anasankha kugwiritsa tchito kampani ya mchimwene wawo wa a Honourable Shadreck Namalomba kuti iunikire kuwerengera kwa ma voti ngati ma Auditors. A Namalomba ndi mneneri wa DPP, yemwe alinso mneneri wa mtsogoleri wa DPP a Peter Mutharika. President wopumayu ndi atsibweni awo a Dr. Kabambe.

    China chofuna kuganizira mwakuya. Zotsatira za Dr. Kabambe zinali 636; mavoti 21 anapita kwa Dr Patricia Kaliati, 22 kwa Dr Matthews Mtumbuka, ndi 26 kwa a Newton Kambala. Ena akambapo kuti izizi zikuoneka ngati kuti mavoti awawa anali okoza kale ndipo chisankho chinangopangika momata anthu mphula mmaso. Kunena zoona ngakhale izizi zingatengedwe ngati nkhamba kamwa chabe koma ndikhani zomwe zikhoza kuononga chipani cha UTM maka pamene dziko la Malawi likupita kuzisankho chaka chamawachi. Enaso akambapo kuti zikhoza kutheka kuti ndalama zinagwiritsidwa ntchito pogula ngakhale anthu amene amayendetsa chisankhochi kuphatikizapo ma monita.

    Chodandaulitsa china ndichakuti ngakhale atolankhani akuoneka kuti alibe chidwi chopanga kafukufuku pa nkhani zimenezi. Funso mkumati kodi atolankhani angolemphera kugwira ntchito chabe kapena nawo anapatsidwa kena kake pofuna kubisa chilungamo? Sitinganeneretu komano kutsatila bwino mmene ndalama zagwiritsidwira ntchito pakampeni ndi kuti chisankhochi chikomere mbali ina yache sitingatsutse pamaganizo amenewa.

    Monga tanena kale, mu 2025 kuli zisankho za dziko pamene UTM motsogozedwa ndi Dr Kabambe akuyembekezera kukapikisana nawo. Funso mkumati kodi ndi nkhani zimenezi, a Malawi ali okozeka kukhulupirira kuti UTM ndi Dr Kabambe ali nkuthekera kulamulira dziko lino mopanda chinyengo, katangale kapena kusolora.

    Chipani cha UTM chikuyenera kuchitapo kanthu kuti chibwezeretse chikhulupiriro chimene a Malawi anali nacho pa chipanichi. Kungokhala ngati palibe chili chonse chachitika ndikosanthandiza.

    Chokhumudwitsa china ndichokuti panopa anthu amene akusapota Dr. Kabambe ali kalikiliki kutukwana ndi kunyazitsa awo omwe zisinayende pa chisankho chimenechi zimeneso zikupangitsa kuti kusakondwa kudzipitililabe. Izizi zilibe mphindu patsogolo la UTM. Nthawi ino nkofunika kuti Dr Kabambe ndi masapota awo adzichepetse ndi kuyesetsa kuwafikira anzawowa monga mayi Kaliati, a Dr Mtumbuka, ndi a Kambala ndi ena maka awo amene ankhala akuyendetsa chipanichi kuyambira 2018 pamodzi ndi malemu Dr Saulos Klaus Chilima.

    Atsogoleri a chipani cha UTM ayenera kuonetsa kugonjera ku chilungamo ndikudzifunsa mafuso awa: Kodi anthu akamapita kuzisankho mu 2025 adzichiona bwanji chipanichi? Kodi a Malawi ankhala okhutila kuti chipanichi chikwanitsa kukwaniritsa masomphenya a mtsogoleri wakale wa UTM malemu Chilima? Apo bii, UTM iyiwale kaye zochita bwino pa zisankho zikubwerazi ndi kulamulira dziko lino.

    Related articles

    LEAVE A REPLY

    Please enter your comment!
    Please enter your name here

    spot_img

    Latest posts