spot_img
Wednesday, January 22, 2025
More
    HomeLatestSindinakumanepo ndi a Chakwera- Kabambe

    Sindinakumanepo ndi a Chakwera- Kabambe

    -

    Wamkulu wakale wa banki yayikulu ya Reserve Bank, a Dalitso Kabambe atsutsa mphekesera zoti wakhala akukumana kangapo konse ndi mtsogoleri wa dziko lino m’busa Lazarus Chakwera, omwenso ndi mtsogoleri wa chipani cha Malawi Congress (MCP).

    A Kabambe, omwenso ndi m’modzi mwa anthu omwe akufuna mpando wa mtsogoleri ku chipani chachikulu chotsutsa boma m’dziko muno cha DPP, ati iwo sanakumanepo ndi a Chakwera m’moyo wawo onse.

    Iwo anena izi kutsatira zomwe masamba ena amchezo akukamba zoti a Chakwera akufuna kusankha a Kabambe ngati Nduna ya Zachuma kutsatira mkumano omwe awiriwa anali nawo muchipinda chomata.

    Koma poyankhapo pa mphekesera zi kudzera pa tsamba lawo lamchezo, a Dr. Kabambe ati anthu omwe akufalitsa izi angofuna kuyambanitsa anthu komanso kugawa chipani cha DPP.

    “Ndafuna kukudziwitsani anthu nonse okonda ndikutsatila chipani cha DPP ndi a Malawi nonse kuti nkhani zikukambidwa mumasamba amchezo kuti ndakumana kapena kuti ndakhala ndikukumana ndi a President a dziko lino Dr Lazarus Chakwera ndibodza la mkunkhuniza lomwe akufalitsa ndi anthu ofuna kuyambanitsa anthu komanso kugawa chipani cha DPP.

    “Ine sindinayambe ndakumanapo ndi a President a dziko lino ndipo ndilibe ma plan ena ali onse pa nkhani ina ili yonse yokhudza mgwirizano ndi chipani cha MCP,” anatero a Kabambe

    Katswiri pa nkhani za chuma yu, Dr. Kabambe atsindika kuti iwo ndi membala wa DPP ndipo ali nga nga nga pa mbuyo pa mtsogoleri wa chipichi a Peter Mutharika.

    “Ine ndi membala wa DPP ndipo ndikugwira ntchito ndi DPP, ndipo ndidzakhala wa DPP motsogozedwa ndi yemwe ndi mtsogoleri wachipanichi, His Excellency Prof. Arthur Peter Mutharika.

    “Chipani cha DPP ndichipani chomwe chimayendetsedwa ndi nsanamila za chitukuko, chilungamo komanso chitetezo, chotelo izi ndi mfundo zothandiza kumanga democracy zomwe ndi mfundo zomwe ndimagwirizana nazo.”

    Pothilirapo ndemanga pa momwe chaka cha 2023 chinalili, a Kabambe ati chaka chatha chinali chaka chowawa kwambiri kwa a Malawi ochuluka maka kwa omwe amakhala m’midzi komanso omwe ndi osowa.

    “Chaka cha 2023 chinali chamazunzo ndi zobetchela zambiri kwa a Malawi, monga kukwera mitengo kwa zinthu, kugwa kwa ndalama yathu ya Kwacha, kukwera mtengo wa chimanga komanso kusowa kumene ndi kusowa kwa mafuta. Koma tithokoze Mulungu kuti watisungabe ndikutilowetsa mu chaka chatsopanochi” Iwo anatero.

    Malingana ndi a Kabambe, chaka chino cha 2024, chipereka mwayi kwa iwo komanso a Malawi kukhala ndi nthawi yoyang’ana komwe achokela, komwe adutsa, ndikomwe akupita, maaka podziwa kuti posachedwapa mu chaka cha 2025 a Malawi akhale akuponya vote yosankha President komanso adindo ena.

    Related articles

    LEAVE A REPLY

    Please enter your comment!
    Please enter your name here

    spot_img

    Latest posts